10. Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,
11. Pitani pakati pa cigono, nimulamulire anthu, ndi kuti, Mudzikonzeretu kamba, pakuti asanapite masiku atatu mudzaoloka Yordano uyu, kulowa ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, likhale lanu lanu.
12. Ndipo Yoswa anati kwa Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la Manase logawika pakati, ndi kuti,
13. Kumbukilani mau amene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani inu, kuti, Yehova Mulungu wanu akupatsani mpumulo, nadzakupatsani dziko lino.