1. NDIPO mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti,
2. Nyamuka, pita ku Nineve, mudzi waukuruwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti coipa cao candikwerera pamaso panga.
3. Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako combo comuka ku Tarisi, napereka ndalama zace, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisi kuzemba Yehova.
4. Koma Yehova anautsa cimphepo cacikuru panyanja, ndipo panali namondwe wamkuru panyanja, ndi combo cikadasweka.