Yohane 7:27-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Koma ameneyo tidziwa uko acokera: koma Kristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko acokera.

28. Pamenepo Yesu anapfuula m'Kacisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndicokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.

29. Ine ndimdziwa iye; cifukwa ndiri wocokera kwa iye, nandituma Ine Iyeyu.

30. Pamenepo anafuna kumgwira iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, cifukwa nthawi yace siinafike.

31. Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira iye; ndipo ananena, Pamene Kristu akadza kodi adzacita zizindikilo zambiri zoposa zimene adazicita ameneyo?

Yohane 7