22. Cifukwa ca ici Mose, anakupatsani inu mdulidwe (si kuti ucokera kwa Mose, koma kwa, makolo); ndipo mudula munthu tsiku la Sabata.
23. Ngati munthu alandira mdulidwe tsiku la Sabata, kuti cilamulo ca Mose cingapasulidwe; kodi mundikwiyira Ine, cifukwa ndamciritsadi munthu tsiku la Sabata?
24. Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani ciweruziro colungama.
25. Pamenepo ena a iwo a ku Yerusalemu ananena, Kodi suyu amene afuna kumupha r
26. ndipo taona amalankhula poyera, ndipo sanena kanthu kwa iye. Kapena kodi akuru adziwa ndithu kuti ndiye Kristu ameneyo?
27. Koma ameneyo tidziwa uko acokera: koma Kristu pamene akadzadza, palibe mmodzi adzadziwa uko acokera.
28. Pamenepo Yesu anapfuula m'Kacisi, alikuphunzitsa ndi kunena, Mundidziwa Ine, ndiponso mudziwa uko ndicokera; ndipo sindinadza Ine ndekha, koma iye wondituma Ine amene inu simumdziwa, ali woona.
29. Ine ndimdziwa iye; cifukwa ndiri wocokera kwa iye, nandituma Ine Iyeyu.
30. Pamenepo anafuna kumgwira iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, cifukwa nthawi yace siinafike.
31. Koma ambiri a m'khamu la anthu anakhulupirira iye; ndipo ananena, Pamene Kristu akadza kodi adzacita zizindikilo zambiri zoposa zimene adazicita ameneyo?
32. Afarisi anamva khamu la anthu ling'ung'udza zimenezi za iye; ndipo ansembe akulu ndi Afarisi anatuma anyamata kuti akamgwire iye.
33. Pamenepo Yesu anati, Katsala kanthawi ndiri ndi inu, ndipo ndimuka kwa iye wondituma Ine.
34. Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndiri Ine, inu simungathe kudzapo.
35. Cifukwa cace Ayuda anati mwa iwo okha, Adzanka kuti uyu kuti ife sitikampeza iye? kodi adzamuka kwa Ahelene obalalikawo, ndi kuphunzitsa Ahelene?
36. Mau awa amene ananena ndi ciani, Mudzandifunafuna osandipeza Ine: ndipo pomwe ndiri Ine, inu simungathe kudzapo?
37. Koma tsiku lomariza, lalikurulo la phwando, Yesu anaimirira napfuula, ndi kunena, Ngati pali munthu akumva Ludzu, adze kwa Ine, namwe.
38. Iye wokhulupirira Ine, monga cilembo cinati, Mitsinje ya madzi amoyo idzayenda, kuturuka m'kati mwace.
39. Koma 1 ici anati za Mzimu, amene iwo akukhulupirira iye anati adzalandire; pakuti Mzimu panalibe pamenepo, cifukwa Yesu sanalemekezedwa panthawi pomwepo.
40. Pamenepo ena a khamulo pakumva mau awa, ananena, 2 Mnene riyo ndi uyu ndithu.
41. Ena ananena, 3 Uyu ndi Kristu, Koma ena ananena, Kodi Kristu adza kuturuka m'Galileya?