Yohane 16:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma ndinena Ine coonadi ndi inu; kuyenera kwa inu kuti ndicoke Ine; pakuti ngati sindicoka, Nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.

8. Ndipo atadza Iyeyo, adzatsutsa dziko lapansi za macimo, ndi za cilungamo, ndi za ciweruziro;

9. za macimo, cifukwa sakhulupirira Ine;

10. za cilungamo, cifukwa ndinka kwa Atate, ndipo simundionanso;

11. za ciweruziro, cifukwa mkuru wa dziko ili lapansi waweruzidwa.

12. Ndiri nazo zambirinso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.

13. Koma atadza Iyeyo, Mzimu wa coonadi, adzatsogolera inu m'coonadi conse; pakuti sadzalankhula za iye mwini; koma zinthu ziri zonse adzazimva, adzazilankhula; ndipo zinthu zirinkudza adzakulalikirani.

14. Iyeyo adzalemekeza Ine; cifukwa adzatenga za mwa Ine, nadzalalikira kwa inu.

Yohane 16