Yohane 16:24-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Kufikira tsopano simunapempha kanthu m'dzina langa; pemphani, ndipo mudzalandira, kuti cimwemwe canu cikwaniridwe.

25. Zinthu izi ndalankhula ndi inu m'mafanizo; ikudza nthawi imene sindidzalankhula ndi inu m'mafanizo, koma ndidzakulalikirani inu momveka za Atate.

26. Tsiku limenelo mudzapempha m'dzina langa; ndipo sindinena kwa inu kuti Ine ndidzafunsira inu kwa Atate;

27. pakuti Atate yekha akonda inu, cifukwa inu mwandikonda Ine, ndi kukhulupirira kuti Ine ndinaturuka kwa Atate.

28. Ndinaturuka mwa Atate, ndipo ndadza ku dziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.

Yohane 16