Yohane 12:8-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pakuti osauka muli nao pamodzi ndi inu nthawi zonse; koma simuli ndi Ine nthawi zonse.

9. Pamenepo khamu lalikuru la Ayuda Iinadziwa kuti ali pomwepo; ndipo anadza, si cifukwa: ca Yesu yekha, koma kuti adzaone Lazaro, amene adamuukitsa kwa akufa.

10. Koma ansembe akulu anapangana kuti akaphe Lazaronso;

11. pakuti ambiri a Ayuda anacoka cifukwa ca iye, nakhulupirira Yesu.

12. M'mawa mwace khamu lalikuru la anthu amene adadza kuphwando, pakumva kuti Yesu alinkudza ku Yerusalemu,

13. anatenga makwata a kanjedza, naturuka kukakomana ndi iye, napfuula, Hosana; wolemekezeka iye wakudza m'dzina la Ambuye, ndiye Mfumu ya Israyeli.

14. Koma Yesu, m'mene adapeza kaburu anakhala pamenepo; monga mulembedwa:

15. Usaope, mwana wamkazi wa Ziyoni; taona Mfumu yako idza wokhala pa mwana wa buru.

Yohane 12