Yohane 12:33-42 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Koma ananena ici ndi kuzindikiritsa imfa yanji akuti adzafa nayo.

34. Pamenepo khamulo linayankha iye, Tidamva ife m'cilamulo kuti Kristu akhala ku nthawi yonse; ndipo Inu munena bwanji, kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa? Mwana wa munthu amene ndani?

35. Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. 1 Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako,

36. 2 Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako.Izi Yesu analankhula, nacoka nawabisalira.

37. Koma angakhale adacita zizindikilo zambiri zotere pamaso pao iwo sanakhulupirira iye;

38. kuti mau a Yesaya mneneri akakwaniridwe, amene anati,3 Ambuye, wakhulupirira ndani kulalikira kwathu?Ndipo mkono wa Ambuye wabvumbulutsidwa kwa yani?

39. Cifukwa ca ici sanathe kukhulupira, pakuti Yesaya anatinso,

40. 4 Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao;Kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima,Nangatembenuke,Ndipo ndingawaciritse.

41. 5 Izi anati Yesaya, cifukwa anaona ulemerero wace; nalankhula za iye.

42. Kungakhale kotero, ambiri a mwa akuru anakhulupirira iye; koma 6 cifukwa ca Afarisi sanabvomereza, kuti angaletsedwe m'sunagoge,

Yohane 12