Yohane 1:33-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo sindinamdziwa iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa iye, 9 yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera.

34. Ndipo ndaona ine, ndipo ndacita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.

35. M'mawa mwacenso analikuimirira Yohane ndi awiri a akuphunzira ace;

36. ndipo poyang'ana Yesu alikuyenda, anati, 10 Onani Mwanawankhosa wa Mulungu!

37. Ndipo akuphunzira awiriwo anamva iye alinkulankhula, natsata Yesu.

38. Koma Yesu anaceuka, napenya iwo alikumtsata, nanena nao, Mufuna ciani? Ndipo anati kwa iye, Rabi (ndiko kunena posandulika, Mphunzitsi), mukhala kuti?

39. Nanena nao, Tiyeni, mukaone, Pamenepo anadza naona kumene anakhala; nakhala ndi iye tsiku lomwelo; panali monga ora lakhumi.

40. Andreya mbale wace wa Simoni Petro anali mmodzi wa awiriwo, anamva Yohane, namtsata iye.

Yohane 1