2. Zoona, ndidziwa kuti ciri cotero.Koma munthu adzakhala walungama bwanji kwa Mulungu?
3. Akafuna Iye kutsutsana naye,Sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa cikwi.
4. Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikuru;Ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?
5. Ndiye amene asuntha mapiri, osacidziwa iwo,Amene amagubuduza mu mkwiyo wace.
6. Amene agwedeza dziko lapansi licoke m'malo mwace,Ndi mizati yace injenjemere.