Yobu 9:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2. Zoona, ndidziwa kuti ciri cotero.Koma munthu adzakhala walungama bwanji kwa Mulungu?

3. Akafuna Iye kutsutsana naye,Sadzambwezera Iye mau amodzi onse mwa cikwi.

4. Ndiye wa mtima wanzeru, ndi wa mphamvu yaikuru;Ndaniyo anadziumitsa mtima pa Iye, nakhala nao mtendere?

Yobu 9