Yobu 2:12-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndipo pokweza maso ao ali kutali, sanamdziwa, nakweza mau ao, nalira; nang'amba yense maraya ace, nawaza pfumbi kumwamba ligwe pamitu pao.

13. Nakhala pansi pamodzi naye panthaka masiku asanu ndi awiri usana ndi usiku, palibe mmodzi ananena naye kanthu, popeza anaona kuti kuwawaku nkwakukuru ndithu.

Yobu 2