1. Ndipo Yehova anati kwa ine, Tenga iwe polembapo papakuru, nulembe pamenepo ndi malembedwe odziwika, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza,
2. Ndipo ndidzadzitengera ine mboni zokhulupirika, Uriya wansembe, ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.
3. Ndipo ndinanka kwa mneneri wamkazi; ndipo iye anatenga pakati nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, Uche dzina lace, Kangazakufunkha Fulumirakusakaza.
4. Cifukwa kuti mwana asakhale ndi nzeru yakupfuula, Atate wanga, ndi Amai wanga, cuma ca Damasiko ndi cofunkha ca Samariya cidzalandidwa pamaso pa mfumu ya Asuri.