10. Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani cifukwa ca iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro;
11. kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mabere a zitonthozo zace; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wace.
12. Pakuti atero Yehova, Taonani ndidzamfikitsira mtendere ngati mtsinje, ndi ulemerero wa amitundu ngati mtsinje wosefukira. Inu mudzayamwa, ndi kunyamulidwa pambali, ndi kululuzidwa pa maondo,
13. Monga munthu amene amace amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima m'Yerusalemu.
14. Ndipo mudzaciona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ace, ndipo adzakwiyira adani ace.