Yesaya 5:18-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zacabe, ndi cimo ngati ndi cingwe ca gareta;

19. amene ati, Mlekeni iye akangaze, mlekeni iye afulumize nchito yace kuti ife tione; ndipo lekani uphungu wa Woyera wa Israyeli uyandikire, udze kuti tiudziwe!

20. Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!

21. Tsoka kwa iwo amene adziyesera anzeru ndi ocenjera!

22. Tsoka kwa iwo amene ali a mphamvu yakumwa vinyo, ndi anthu olimba akusanganiza zakumwa zaukali;

23. amene alungamitsa woipa pa cokometsera mlandu, nacotsera wolungama cilungamo cace!

Yesaya 5