Yesaya 5:13-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Cifukwa cace anthu anga amuka m'nsinga, cifukwa ca kusowa nzeru; ndi amuna ao olemekezeka ali ndi njala, ndi khamu lao lauma kukhosi.

14. Ndipo manda akuza cilakolako cace, natsegula kukamwa kwace kosayeseka; ndi ulemerero wao, ndi unyinji wao, ndi phokoso lao, ndi iye amene akondwerera mwa iwo atsikira mommo.

15. Munthu wonyozeka waweramitsidwa, ndi munthu wochuka watsitsidwa, ndi maso a wodzikweza atsitsidwa;

16. koma Yehova wa makamu wakwezedwa m'ciweruziro, ndipo Mulungu Woyera wayeretsedwa m'cilungamo.

17. Pamenepo ana a nkhosa adzadyapo ngati m'busa mwao, ndi malo a bwinja a zonenepa zacilendo zidzadyapo.

18. Tsoka kwa iwo amene akoka mphulupulu ndi zingwe zacabe, ndi cimo ngati ndi cingwe ca gareta;

Yesaya 5