1. Koma tsopano, imva Yakobo, mtumiki wanga, ndi Israyeli, amene ndakusankha;
2. atero Yehova, amene anakutenga iwe, nakuumba kucokera m'mimba, amene adzathangata iwe. Usaope Yakobo, mtumiki wanga ndi iwe, Yesuruni, amene ndakusankha iwe.
3. Pakuti ndidzathira madzi pa dziko limene liribe madzi, ndi mitsinje pa nthaka youma; ndidzathira mzimu wanga pa mbeu yako, ndi mdalitso wanga pa obadwa ako;
4. ndipo iwo adzaphuka pakati pa maudzu, ngati msondodzi m'mphepete mwa madzi.