Yesaya 43:26-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe.

27. Atate wako woyamba anacimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine.

28. Cifukwa cace ndidzaipitsa akuru a kacisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israyeli akhale citonzo.

Yesaya 43