Yesaya 40:28-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Kodi iwe sunadziwe? kodi sunamve? Mulungu wacikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zace sizisanthulika.

29. Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.

30. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu:

31. koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga kuma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Yesaya 40