1. Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu.
2. Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimupfuulire kwa iye, kuti nkhondo yace yatha, kuti kuipa kwace kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, cifukwa ca macimo ace onse.
3. Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti se khwalala la Mulungu wathu.
4. Cigwa ciri conse cidzadzazidwa, ndipo phiri liri lonse ndi citunda ciri conse zidzacepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala;