Yesaya 27:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lace lolimba ndi lalikuru ndi lamphamvu adzalanga nangumi njoka yotamanga, ndi nangumi njoka yopindika-pindika; nadzapha cing'ona cimene ciri m'nyanja.

2. Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, yimbani inu za uwo.

3. Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.

Yesaya 27