Yesaya 21:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mucingamire akumva ludzu ndi madzi; okhala m'dziko la Tema ananka kukomana ndi othawa ndi cakudya cao.

15. Pakuti iwo anathawa malupanga, malupanga osololedwa, ndi mauta-olifuka ndi nkhondo yobvuta.

16. Pakuti Ambuye ana tero kwa ine, Cisanapite caka malinga ndi zaka za wolembedwa nchito ulemerero wonse wa Kedara udzagoma;

17. ndi otsala amauta, ngwazi za ana a Kedara zidzacepa, pakuti Yehova Mulungu wa Israyeli wanena.

Yesaya 21