14. ndi pa mapiri onse atari, ndi pa zitunda zonse zotukulidwa;
15. ndi pa nsanja zazitari zonse, ndi pa macemba onse;
16. ndi pa ngalawa zonse za Tarisi, ndi pa zithunzithunzi zonse zokondweretsa.
17. Ndipo kudzikweza kwa munthu kudzaweramitsidwa pansi, kudzikuza kwa munthu kudzatsitsidwa; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.
18. Ndimo mafano adzapita psiti.
19. Anthu adzalowa m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'maenje apansi, kuthawa kuopsya kwa Yehova, ndi ulemerero wacifumu wace, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.