22. Ndipo Yehova adzakantha Aigupto kukantha ndi kuciritsa; ndipo iwo adzabwerera kwa Yehova, ndipo Iye adzapembedzedwa ndi iwo, nadzawaciritsa.
23. Tsiku limenelo padzakhala khwalala locokera m'Aigupto kunka ku Asuri, ndipo M-asuri adzafika ku Aigupto, ndi M-aigupto adzafika ku Asuri, ndipo Aaigupto adzapembedzera pamodzi ndi Aasuri.
24. Tsiku limenelo Israyeli ndi Aigupto ndi Asuri atatuwa, adzakhala mdalitso pakati pa dziko lapansi;
25. pakuti Yehova wa makamu wadalitsa iwo, ndi kuti, Odalitsika Aigupto anthu anga, ndi Asuri nchito ya manja anga, ndi Israyeli colowa canga.