6. Ife tinamva kunyada kwa Moabu, kuti iye ali wonyada ndithu; ngakhale kudzitama kwace, ndi kunyada kwace ndi mkwiyo wace; matukutuku ace ali acabe.
7. Cifukwa cace Moabu adzakuwa cifukwa ca Moabu, onse adzakuwa; cifukwa ca maziko a Kirihareseti mudzalira maliro, osautsidwa ndithu.
8. Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibimai; ambuye a mitundu atyolatyola mitengo yosankhika yace; iwo anafikira ngakhale ku Yazeri, nayendayenda m'cipululu; nthambi zace zinatasa, zinapitima panyanja.