Yesaya 16:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tumizani inu ana a nkhosa kwa wolamulira wa dziko kucokera ku Sela kunka kucipululu, mpaka ku phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.

2. Pakuti ana akazi a Moabu adzakhala pa madooko a Arinoni, ngati mbalame zoyendayenda, ngati cisa cofwancuka.

3. Citani uphungu, weruzani ciweruziro; yesa mthunzi wako monga usiku pakati pa usana; bisa opitikitsidwa, osaulula woyendayenda.

4. Opitikitsidwa a Moabu akhale ndi iwe, khala iwe comphimba pamaso pa wofunkha; pakuti kumpambapamba kwalekeka, kufunkha kwatha, opondereza atsirizika m'dziko.

Yesaya 16