Yesaya 13:20-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo; M-arabu sadzamanga hema wace pamenepo; abusa sadzagonetsa makamu ao kumeneko.

21. Koma zirombo za m'cipululu zidzagona pamenepo; nyumba zao zidzadzala ndi zakukuwa; ndipo nthiwatiwa zidzakhala pamenepo, ndipo atonde adzajidimuka pamenepo,

22. Ndipo mimbulu idzalira m'maboma ao, ndi ankhandwe m'manyumba ao abwino; ndi nthawi yace iyandikira, ndi masiku ace sadzacuruka.

Yesaya 13