18. Mauta ao adzatha anyamata; ndipo sadzacitira cisoni cipatso ca mimba; diso lao silidzaleka ana.
19. Ndipo Babulo, ulemerero wa maufumu, mudzi wokongolawo Akasidi anaunyadira, adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora.
20. Anthu sadzakhalamo konse, sadzakhalamo mbadwo ndi mbadwo; M-arabu sadzamanga hema wace pamenepo; abusa sadzagonetsa makamu ao kumeneko.