Yesaya 1:11-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Nditani nazo nsembe zanu zocurukazo? ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa ana a nkhosa, ngakhale wa atonde.

12. Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna cimeneci m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga?

13. Musadze nazonso, nsembe zacabecabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano.

14. Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi za mapwando anu mtima wanga uzida; zindibvuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.

15. Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pocurukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.

16. Sambani, dziyeretseni; cotsani macitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kucita zoipa;

17. phunzirani kucita zabwino; funani ciweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.

Yesaya 1