15. cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Taonani, ndidzadyetsa anthu awa civumulo, ndi kuwamwetsa madzi andulu.
16. Ndidzawabalalitsanso mwa amitundu, amene iwo kapena makolo ao sanawadziwa; ndipo ndidzatumiza lupanga, liwatsate mpaka ndawatha.
17. Atero Yehova wa makamu, Kumbukirani inu, ndi kuitana akazi akulira, adze; aitaneni akazi ocenjera, kuti adze;
18. afulumire, atikwezere ife mau a maliro, kuti maso athu agwe misozi, ndi zikope zathu ziyendetse madzi.
19. Pakuti mau a kulira amveka m'Ziyoni, Tafunkhidwa, tanyazitsidwa, pakuti tasiya dziko, pakuti agwetsa zokhalamo zathu.