32. Cifukwa cace, taonani, masiku alikudza, ati Yehova, ndipo sadzachedwanso Tofeti, kapena Cigwa ca mwana wa Hinomu, koma Cigwa ca Kuphera; pakuti adzataya m'Tofeti, kufikira malo akuikamo adzasowa.
33. Ndipo mitembo ya anthu awa idzakhala zakudya za mbalame za mlengalenga, ndi za zirombo za dziko lapansi; palibe amene adzaziopsa.
34. Ndipo ndidzaletsa m'midzi ya Yuda, ndi m'miseu ya Yerusalemu, mau akukondwa ndi mau akusekera, ndi mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi; pakuti dziko lidzasanduka bwinja.