8. Babulo wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zace bvunguti, kapena angacire.
9. Tikadaciritsa Babulo koma sanacire; mumsiye iye, tipite tonse yense ku dziko lace; pakuti ciweruziro cace cifikira kumwamba, cinyamulidwa mpaka kuthambo,
10. Yehova waturutsa cilungamo cathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni nchito ya Yehova Mulungu wathu.
11. Nolani mibvi; gwirani zolimba zikopa; Yehova waukitsa mtima wa mafumu a Amedi; cifukwa alingalirira Babulo kuti amuononge; pakuti ndi kubwezera cilango kwa Yehova; kubwezera cilango cifukwa ca Kacisi wace.