6. Thawani pakati pa Babulo, yense apulumuke moyo wace; musathedwe m'coipa cace; pakuti ndi nthawi ya kubwezera cilango; Yehova adzambwezera iye mphotho yace.
7. Babulo wakhala cikho cagolidi m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wace; cifukwa cace amitundu ali ndi misala.
8. Babulo wagwa dzidzidzi naonongedwa; mumkuwire iye; mutengere zowawa zace bvunguti, kapena angacire.
9. Tikadaciritsa Babulo koma sanacire; mumsiye iye, tipite tonse yense ku dziko lace; pakuti ciweruziro cace cifikira kumwamba, cinyamulidwa mpaka kuthambo,
10. Yehova waturutsa cilungamo cathu; tiyeni tilalikire m'Ziyoni nchito ya Yehova Mulungu wathu.