32. Ndipo ngamila zao zidzakhala zofunkha, ndi unyinji wa ng'ombe zao udzakhala wolanda; ndipo ndidzabalalitsira ku mphepo zonse iwo amene ameta m'mbali mwa tsitsi lao; ndipo ndidzatenga tsoka lao ku mbali zao zonse, ati Yehova.
33. Ndipo Hazori adzakhala mokhalamo ankhandwe, bwinja lacikhalire; simudzakhalamo munthu, simudzagonamo mwana wa munthu.
34. Mau a Yehova amene anafika kwa Yeremiya mneneri, onena za Elamu poyamba kulamulira Zedekiya mfumu ya Yuda, kuti,
35. Yehova wa makamu atero: Taonani, ndidzatyola uta wa Elamu, ndiwo mtima wa mphamvu yao.
36. Pa Elamu ndidzatengera mphepo zinai ku mbali zinai za mlengalenga, ndidzamwaza iwo ku mphepo zonsezo; ndipo sikudzakhala mtundu kumene opitikitsidwa a Elamu sadzafikako.