Yeremiya 49:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo Edomu adzakhala cizizwitso; ndipo yense wakupitapo adzazizwa, ndipo adzatsonyera zobvuta zace zonse.

18. Monga m'kupasuka kwa Sodomu ndi Gomora ndi midzi inzace, ati Yehova, munthu ali yense sadzakhala m'menemo, mwana wa munthu ali yense sadzagona m'menemo.

19. Taona, wina adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wocokera ku Yordano wosefuka; koma dzidzidzi ndidzamthamangitsa amcokere; ndipo ali yense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wace, pakuti wakunga Ine ndani? adzandiikira nthawi ndani? ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?

20. Cifukwa cace tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Edomu; ndi zimene walingalirira okhala m'Temani, ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.

Yeremiya 49