Yeremiya 48:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Za Moabu Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Tsoka Nebo! pakuti wapasuka; Kiriyataimu wacitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lacitidwa manyazi lapasudwa.

2. Palibenso kutamanda Moabu; m'Hesiboni anamlingiririra zoipa, ndi kuti, Tiyeni, tiwathe asakhalenso mtundu waanthu. Iwenso, Madimeni, udzatontholetsedwa, lupanga lidzakulondola iwe.

3. Mau amveka kucokera ku Horonaimu, kufunkha ndi kuononga kwakukuru!

4. Moabu waonongedwa; ang'ono ace amveketsa kulira.

Yeremiya 48