1. Ndipo panali pamene Yeremiya anatha kunena kwa anthu onse mau onse a Yehova Mulungu wao, amene anamtuma iye nao Yehova Mulungu wao, mau onse amenewo,
2. pamenepo ananena Azariya mwana wace wa Hosaya, ndi Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi anthu onse odzikuza, nati kwa Yeremiya, Unena zonama; Yehova Mulungu wathu sanakutumiza iwe kudzanena, Musalowe m'Aigupto kukhala m'menemo;