1. Ndipo akazembe onse a nkhondo, ndi Yohanani mwana wace wa Kareya, ndi Jezaniya mwana wace wa Hosiya, ndi anthu onse kuyambira wamng'ono, kufikira wamkuru, anayandikira,
2. nati kwa Yeremiya mneneri, Cipembedzero cathu cigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Ambuye Mulungu wanu, cifukwa ca otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;
3. kuti Yehova Mulungu wanu atisonyeze ife njira imene tiyendemo, ndi comwe ticite.
4. Ndipo Yeremiya mneneri anati kwa iwo, Ndamva; taonani, ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga mwa mau anu; ndipo padzakhala kuti ciri conse Yehova adzakuyankhirani, ndidzakufotokozerani; sindidzakubisirani inu kanthu.