26. Ndipo mfumu inauza Yeremeeli mwana wace wa mfumu, ndi Seraya mwana wa Azirieli, ndi Selemiya mwana wa Abidieli, kuti awagwire Baruki mlembi ndi Yeremiya mneneri; koma Yehova anawabisa.
27. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, mfumu itatentha mpukutuwo, ndi mau amene analemba Baruki ponena Yeremiya, kuti,
28. Tenganso mpukutu wina, nulembe m'menemo mau oyamba aja anali mu mpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wautentha.