Yeremiya 30:14-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka.

15. Cifukwa canji ulilira bala lako? kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka, ndakucitira iwe izi.

16. Cifukwa cace iwo akulusira iwe adzalusidwanso; ndi adani ako onse, adzanka kuundende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala cofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.

17. Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; cifukwa anacha iwe wopitikitsidwa, nati, Ndiye Ziyoni, amene kulibe munthu amfuna.

18. Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzacitira cifundo zokhalamo zace, ndipo mudzi udzamangidwa pamuunda pace, ndi cinyumba cidzakhala momwe.

19. Ndipo padzaturuka pa izo mayamikiro ndi mau a iwo okondwerera; ndipo ndidzacurukitsa iwo, sadzakhala owerengeka; ndidzawacitiranso ulemu, sadzacepa.

20. Ana aonso adzakhala monga kale, ndipo msonkhano wao udzakhazikika pamaso panga, ndipo ndidzalanga onse amene akupsinja iwo.

Yeremiya 30