Yeremiya 30:12-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Pakuti atero Yehova, Kulaswa kwako kuti kosapoleka ndi bala lako liri lowawa.

13. Palibe amene adzanenera mlandu wako, ulibe mankhwala akumanga nao bala lako.

14. Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka.

15. Cifukwa canji ulilira bala lako? kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka, ndakucitira iwe izi.

16. Cifukwa cace iwo akulusira iwe adzalusidwanso; ndi adani ako onse, adzanka kuundende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala cofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.

17. Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; cifukwa anacha iwe wopitikitsidwa, nati, Ndiye Ziyoni, amene kulibe munthu amfuna.

Yeremiya 30