Yeremiya 22:8-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo amitundu ambiri adzapita pa mudzi uwu, nadzati yense kwa mnzace, Yehova anatero nao mudzi waukuru uwu cifukwa ninji?

9. Ndipo adza yankha, Cifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu yina, ndi kuitumikira.

10. Musamlirire wakufa, musacite maliro ace; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.

Yeremiya 22