1. Yehova atero: Tsikira ku nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi kunena komweko mau awa,
2. ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.
3. Yehova atero: Citani ciweruzo ndi cilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musacite coipa, musamcitire mlendo ciwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosacimwa pamalo pano.
4. Pakuti ngati mudzacitadi ici pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wacifumu wa Davide, okwera m'magareta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ace, ndi anthu ace.