Yeremiya 15:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuti ndani adzakucitira iwe cisoni, Yerusalemu? ndani adzakulirira iwe? ndani adzapatukira kudzafunsa za mkhalidwe wako?

6. Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; cifukwa cace ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.

7. Ndawakupa ndi mkupo m'zipata za dziko; ndacotsa ana ao, ndasakaza anthu anga; sanabwerere kuleka njira zao.

8. Amasiye ao andicurukira Ine kopambana mcenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.

9. Mkazi amene anabala asanu ndi awiri walefuka; wapereka moyo; dzuwa lace lalowa usana ulipobe; wanyazitsidwa, wathedwa nzeru; otsala ao ndidzapereka kulupanga pamaso pa adani ao, ati Yehova.

10. Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletsa paphindu; koma iwo onse anditemberera.

11. Yehova anati, Ndithu ndidzakulimbitsira iwe zabwino; ndithu ndidzapembedzetsa mdani kwa iwe nthawi ya zoipa ndi nthawi yansautso.

12. Kodi angathe munthu kutyola citsulo, citsulo ca kumpoto, ndi mkuwa?

Yeremiya 15