Yeremiya 15:20-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndidzakuyesa iwe linga lamkuwa la anthu awa; ndipe adzamenyana ndi iwe, koma iwo sadzakuposa iwe; pakuti Ine ndiri ndi iwe kuti ndikupulumutse ndi kukulanditsa iwe, ati Yehova.

21. Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsya.

Yeremiya 15