Yeremiya 14:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Atero Yehova kwa anthu awa, Comwecoakonda kusocerera; sanakaniza mapazi ao; cifukwa cace. Yehova sawalandira; tsopano adzakumbukira coipa cao, nadzalanga zocimwa zao.

11. Ndipo Yehova anati kwa ine, Usapempherere anthu awa zabwino.

12. Pamene asala cakudya, sindidzamva kupfuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi cirala, ndi caola.

13. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Yehova! taonani, aneneri ati kwa iwo, Simudzaona lupanga, simudzakhala ndi cirala; koma ndidzakupatsani mtendere weniweni mommuno.

14. Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi cinthu cacabe, ndi cinyengo ca mtima wao.

Yeremiya 14