3. Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine nthawi yaciwiri, kuti,
4. Tenga mpango umene unaugula, umene uli m'cuuno mwako, nuuke, nupite ku Firate, nuubise m'menemo m'phanga la m'mwala.
5. Ndipo ndinapita, ndinaubisa pa Firate, monga Yehova anandiuza ine.
6. Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Firate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.