8. Koma sanamvera, sanachera khutu lao, koma onse anayenda m'kuumirira kwa mtima wao woipa; cifukwa cace ndinatengera iwo mau onse a pangano ili, limene ndinauza iwo kuti acite, koma sanacita.
9. Ndipo Yehova anati kwa ine, Ciwembu caoneka mwa anthu a Yuda, ndi mwa anthu okhala m'Yerusalemu.
10. Abwerera kucitanso zoipa za makolo ao, amene anakana kumva mau anga; ndipo atsata milungu yina kuti aitumikire; nyumba ya Israyeli ndi nyumba ya Yuda zaswa pangano langa limene ndinapangana ndi makolo ao.