23. Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ace.
24. Yehova, mundilangize, koma ndi ciweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti.
25. Tsanulirani ukali wanu pa amitundu osakudziwani Inu, ndi pa mabanja osaitana dzina lanu; pakuti anadya Yakobo, inde, anamudya namutha, napasula mokhalamo mwace.