Yakobo 5:7-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwace kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira cipatso cofunikatu ca dziko, ndi kuleza mtima naco kufikira cikalandira mvula ya myundo ndi masika,

8. Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwace kwa Ambuye kuyandikira.

9. Musaipidwe wina ndi mnzace, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.

10. Tengani, abale, citsanzo ca kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri ameneanalankhulam'dzina la Ambuyeo

Yakobo 5